Isaiah 61:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu mudzatchedwa ansembe a Chauta, ponena za inu anthu adzati ndinu atumiki a Mulungu. Mudzadyerera chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwaŵalanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova, adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu. Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu mudzachedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya cuma ca amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.