Isaiah 61:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m'dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa manyazi awo anali owirikiza; ndi kuti munalandira chitonzo ndi kutukwana, adzakondwera ndi cholowa chawo, tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza, ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi citonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; cifukwa cace iwo adzakhala naco m'dziko mwao colowa cowirikiza, adzakhala naco cikondwerero cosatha.