Isaiah 62:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tulukani, inu a mu Yerusalemu, inde tulukani mumzindamo, mukakonze mseu woti anthu anu obwerera kwao aziyendamo. Mulambule mseu waukulu, ndipo muchotsemo miyala. Mukweze mbendera kuti mitundu ya anthu iziwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; chotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tulukani, dutsani pa zipata! Konzerani anthu njira. Lambulani, lambulani msewu waukulu! Chotsani miyala. Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; cotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.