Isaiah 62:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta walengeza ku dziko lonse lapansi zakuti muuze anthu a ku Yerusalemu kuti, “Chipulumutso chanu chikubwera. Chauta akubwera ndi mphotho yake, akubwera nazo zokuyenererani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova walengeza ku dziko lonse lapansi kuti, Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti, “Taonani, chipulumutso chanu chikubwera; Yehova akubwera ndi mphotho yake akubwera nazo zokuyenerani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona cipulumutso cako cifika; taona mphotho yace ali nayo, ndi nchito yace iri pamaso pace.