Isaiah 62:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako amuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mnyamata amakwatira namwali, momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira; monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi, chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako amuna adzakukwama iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.