Isaiah 62:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adalumbira motsimikiza, ndipo adzasunga malumbirowo ndi mphamvu zake. Adati, “Adani ako sadzadyanso tirigu wako, ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova analumbira pa dzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova analumbira atakweza dzanja lake. Anati, “Sindidzaperekanso tirigu wako kuti akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano pakuti unamuvutikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova analumbira pa dzanja lace lamanja, ndi mkono wace wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale cakudya ca adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira nchito;