Isaiah 62:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu amene mudabzala ndi kukolola tiriguyo, ndiye amene mudzadye buledi, ndipo mudzatamanda Chauta. Inu amene munkasamala mitengo yamphesa ndi kumathyola mphesa, ndiye amene mudzamwe vinyo m'mabwalo a Nyumba yanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi ndi kutamanda Yehova, ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo mʼmabwalo a Nyumba yanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamchera adzamumwa m'mabwalo a kacisi wanga.