Isaiah 63:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe iwo adampandukira, namkwiyitsa Mulungu. Motero Chauta adasanduka mdani wao, ndipo adamenyana nawo nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe iwo anawukira ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa cisoni mzimu wace woyera, cifukwa cace Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.