Isaiah 63:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthuwo adakumbuka zamakedzana, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo adafunsa kuti, “Ali kuti tsopano Chautayo amene adapulumutsa anthu ake pamodzi ndi mtsogoleri wao pa nyanja? Ali kuti Chautayo amene adaika mwa anthu ake mzimu wake woyera?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ake, nati, Ali kuti Iye amene anawatulutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lake? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wake woyera pakati pao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana, masiku a Mose mtumiki wake; ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja, pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo? Ali kuti Iye amene anayika Mzimu Woyera pakati pawo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ace, nati, Ali kuti Iye amene anawaturutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lace? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wace woyera pakati pao,