Isaiah 63:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali kuti Chautayo amene adachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Adagaŵa madzi am'nyanja, anthu ake akuwona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene anayendetsa mkono wake waulemerero pa dzanja lamanja la Mose? Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene anayendetsa mkono wace waulemerero pa dzanja lamanja la Mose? amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?