Isaiah 63:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adadzandithandiza. Ndidaŵapondereza ndili wokwiya, magazi ao nkufalikira pa zovala zanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga; ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zovala zanga; ndipo ndadetsa chofunda changa chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, palibe ndi mmodzi yemwe anali nane. Ndinawapondereza ndili wokwiya ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali; magazi awo anadothera pa zovala zanga, ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga: ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zobvala zanga; ndipo ndadetsa copfunda canga conse.