Isaiah 63:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidayang'ana, koma panalibe wondithandiza. Ndidadabwa kwabasi kuti panalibe wondichirikiza. Choncho ndidapambana ndi mphamvu za ine ndekha, unkandilimbitsa ndi mkwiyo wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza. Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza; choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga, ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.