Isaiah 64:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumaŵalandira onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amayesetsa kuyenda monga Inu mufunira. Inde mudatikwiyira, komabe ife tidapitiriza kuchimwa. Takhala ochimwadi nthaŵi yaitali, kodi tidzapulumuka kumene?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nachita chilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinachimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amakumbukira njira zanu. Koma Inu munakwiya, ife tinapitiriza kuchimwa. Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nacita cilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinacimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?