Isaiah 64:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tonsefe tasanduka ngati anthu oipitsidwa, ndipo ntchito zathu zonse zabwino zakhala ngati nsanza zauve. Tonsefe tikufota ngati masamba, tikuuluzika ndi machimo athu, ngati tikuuluzika ndi mphepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa, ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo; tonse tafota ngati tsamba, ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse ziri ngati cobvala codetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.