Isaiah 65:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adati, “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a anthu amene sadandipemphere. Ndinali wokonzeka kuti andipeze anthu amene sadandifunefune. Mtunduwo sudapemphere kwa Ine ngakhale nthaŵi zonse ndinali wokonzeka kuŵayankha kuti, ‘Ine ndili pano, ndikuthandizani.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchula dzina langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu; ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze. Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine, ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo amene sanafunsa za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaira andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunachula dzina langa.