Isaiah 65:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero wopempha madalitso m'dzikomo, adzachita zimenezo kwa Mulungu wolankhula zoona. Ndipo wochita malumbiro m'dzikomo, adzalumbira m'dzina la Mulungu wolankhula zoona, chifukwa choti mavuto akale aiŵalika ndipo achotsedwa pamaso panga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo adzachita zimenezo kwa Mulungu woona; ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo adzalumbira mwa Mulungu woona. Pakuti mavuto akale adzayiwalika ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
comweco iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zobvuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.