Isaiah 65:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya chifukwa cha zimene ndikulenga, pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ici ndicilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ace okondwa.