Isaiah 65:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana sadzafanso ali akhanda, ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zao zonse. Amene adzafe ali a zaka zana limodzi zokha adzaoneka ngati anyamata. Kufa zisanakwane zaka zana limodzi kudzasonyeza kutembereredwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ana sadzafa ali akhanda ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse. Wamngʼono mwa iwo adzafa ali ndi zaka 100. Amene adzalephere kufika zaka 100 adzatengedwa kukhala wotembereredwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ace; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wocimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatembereredwa.