Isaiah 65:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadzamanga nyumbazo kuti anthu ena azikhalamo, ndipo sadzabzala mipesayo kuti anthu ena azidyerera zipatso zake. Anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Ndipo anthu anga osankhidwa adzakondwerera ntchito za manja ao nthaŵi yaitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo, kapena kudzala ndi ena nʼkudya. Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito ya manja awo nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzanka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhalamasiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi nchito za manja ao.