Isaiah 65:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mimbulu ndi anaankhosa zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ng'ombe. Fumbi ndiye lidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa loyera la Ziyoni sipadzakhala chinthu chopweteka kapena choononga,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ngʼombe, koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala chinthu chopweteka kapena chowononga,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi pfumbi lidzakhala cakudya ca njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.