Isaiah 65:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Amauza ena kuti, ‘Khalani panokha, osatiyandikira, chifukwa ndife opatulika.’ Sindingathe kupirira nawo anthu otere. Ukali wanga pa iwo uli ngati moto wosazima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire, chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’ Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga, ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene ati, Ima pa wekha, usadze cifupi ndi ine, pakuti ine ndiri woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.