Isaiah 65:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵalanganso chifukwa cha machimo a makolo ao. Iwowo afukiza lubani pa mapiri a mafano achikunja, ndipo andinyoza Ine pa zitunda zao. Nchifukwa chake ndidzaŵalanga potsata zimene achita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
zoipa zanuzanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandichitira mwano pazitunda; chifukwa chake Ine ndidzayesa ntchito yao yakale ilowe pa chifuwa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi a makolo awo,” akutero Yehova. “Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo, Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata zimene anachita kale.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
zoipa zanu zanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandicitira mwano pazitunda; cifukwa cace Ine ndidzayesa nchito yao yakale ilowe pa cifuwa cao.