Isaiah 65:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Pamene madzi adakalimo m'mphesa, anthu amati, ‘Musaziwononge, zokoma zidakalimo.’ Inenso ndidzaŵatero anthu anga, sindidzaŵaononga onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo, popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’ Inenso chifukwa cha mtumiki wanga; sindidzawononga onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, momwemo ndidzacita cifukwa ca atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.