Isaiah 65:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'banja la Yakobe ndidzatulutsamo zidzukulu, ndipo a m'banja la Yuda adzalandira dziko langa lamapiri ngati choloŵa chao. Anthu anga osankhidwa adzalilandiradi, atumiki anga adzakhala kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatulutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira cholowa chao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo, ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo. Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi, ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaturutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira colowa cao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.