Isaiah 66:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wacifumu, ndi dziko lapansi ndi coikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?