Isaiah 66:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzasangalala poona zimenezi. Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Tsono mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndimathandiza amene amandimvera, ndipo ndimakwiyira adani anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzachiona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ake, ndipo adzakwiyira adani ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu. Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira ndi kuti ndimakwiyira adani anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzaciona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ace, ndipo adzakwiyira adani ace.