Isaiah 66:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, Yehova akubwera ngati moto, ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu; Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake ndi malawi amoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magareta ace adzafanana ndi kabvumvulu; kubwezera mkwiyo wace ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto,