Isaiah 66:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Amene akuti akudzipatula ndi kudziyeretsa pamene akufuna kuchita miyambo yam'minda ija, ali ndi mtsogoleri wao yemwe, nkumadya nyama yankhumba, mbeŵa ndi zonyansa zina, onsewo adzafera limodzi,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatanetsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi chonyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatane tsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi conyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.