Isaiah 66:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ine ndidziwa nchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.