Isaiah 66:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzaika chizindikiro pakati pao. Mwa iwowo padzakhala ena opulumukako amene ndidzaŵatuma kwa anthu a mitundu ina, monga a ku Tarisisi, a ku Puti ndi a ku Ludi, akatswiri a mauta, ndiponso ku Tubala, ku Yavani, ndi ku maiko akutali amene sadamvepo za mbiri yanga kapena kuwona ulemerero wanga. Iwowo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaika cizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisi, kwa Puli ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubali ndi Yavana, ku zisumbu zakutari, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.