Isaiah 66:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adzabwera nawo abale anu onse kuchokera kwa anthu a mitundu yonse, kuti akhale mphatso kwa Ine. Adzabwera nawo ku phiri langa loyera la Yerusalemu, abale anuwo ataŵakweza pa akavalo, abulu, ngamira ndiponso pa magaleta ndi ngolo. Adzabwera nawo monga momwe Aisraele amabwerera ndi zopereka za chakudya ku Nyumba ya Mulungu, atazitenga m'ziŵiya zotsukatsuka,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magareta, ndi m'macila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamila, kudza ku phiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israyeli abwera nazo nsembe zao m'cotengera cokonzeka ku nyumba ya Yehova.