Isaiah 66:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo adzatuluka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mphutsi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo adzaturuka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mbozi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.