Isaiah 66:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera. Kwa iwo nchimodzimodzi kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe kapena kupha munthu, kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe kapena kupha galu, kupereka chopereka cha chakudya kapena kupereka magazi a nkhumba, kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso kapena kupembedza fano. Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna amaphanso munthu, ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa, amaphanso galu. Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya amaperekanso magazi a nkhumba. Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso amapembedzanso fano. Popeza iwo asankha njira zawozawo, ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwana wa nkhosa alingana ndi wotyola khosi la garu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza conunkhira akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zao zao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;