Isaiah 66:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine tsono ndidzaŵagwetsera chilango ndipo ndidzaŵachititsa mantha, chifukwa nditaŵaitana, palibe amene adandiyankha, kapena kutchera khutu pamene ndinkalankhula. Adachita zoipa pamaso panga, adasankhula kuchita zimene zimandinyansa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamve konse; koma anachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene ndisanakondwere nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inenso ndawasankhira chilango chowawa ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija. Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha, pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu. Anachita zoyipa pamaso panga ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamva konse; koma anacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene ndisanakondwere naco.