Isaiah 66:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani mau a Chauta, inu amene mumanjenjemera akamalankhula. Iye akuti, “Abale anu omwe amene amadana nanu nakukanani chifukwa cha dzina langa, amati, ‘Chauta alemekezeke, kuti ife tiwone chimwemwe chanu.’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani mawu a Yehova, inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake: “Abale anu amene amakudani, ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti, ‘Yehova alemekezeke kuti ife tione chimwemwe chanu!’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ace; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja cifukwa ca dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.