Isaiah 66:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani adamvapo zoterezi? Ndani adaziwonapo zoterezi? Kodi dziko nkupangika tsiku limodzi? Kodi mtundu wa anthu nkubadwa tsiku limodzi? Koma Ziyoni adabala ana ake aamuna, atangoyamba kuvutika kumene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani anamva kanthu kotereko? Ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? Pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala anake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani anamvapo zinthu zoterezi? Ndani anazionapo zinthu zoterezi? Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi, kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi? Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa nthawi yomweyo anabereka ana ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani anamva kanthu kotereko? ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala ana ace.