Isaiah 66:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ine ndidzafikitsa anthu anga mpaka nthaŵi yobala, koma osalola kuti abaledi?” Akuterotu Chauta. “Kodi Ine, amene ndili wobalitsa, ndingatseke mimba nthaŵi imeneyo?” Akuterotu Mulungu wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? Ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? Ati Mulungu wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira, koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova. “Kodi ndingatseke mimba pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? ati Mulungu wako.