Isaiah 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Ahazi, mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya, anali mfumu ya ku Yuda, Rezini mfumu ya ku Siriya ndiponso Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya ku Israele, adaadza ku Yerusalemu, kuti adzathire nkhondo mzindawo, koma sadaugonjetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israyeli, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupamnana.