Isaiah 7:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Upemphe chizindikiro kwa Chauta, Mulungu wako. Chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzipemphere wekha cizindikilo ca kwa Yehova Mulungu wako; pempha cam'mwakuya, kapena cam'mwamba.