Isaiah 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nthaŵi imeneyo isanafike, maiko a mafumu aŵiri amene akukuwopsaniwo, adzakhala atasanduka mabwinja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana coipa ndi kusankha cabwino, dziko limene mafumu ace awiri udana nao lidzasyidwa.