Isaiah 7:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chauta adzafikitsa pa inu, pa anthu anu, ndiponso pa banja la bambo wanu, masiku amavuto oti sadakhalepo kuyambira tsiku limene Efuremu adapatukana ndi Yuda. Ndiye kuti adzafikitsa mfumu ya ku Asiriya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efraimu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asuri.