Isaiah 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsiku limenelo Chauta adzalizira khweru Aejipito ndipo adzabwera ambiri ngati ntchentche, zochokera ku mathero a nthambi za mtsinje wa Nailo. Adzaliziranso Aasiriya ndipo adzabwera ambiri ngati njuchi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzaimbira mluzu ntchentche ili m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Ejipito, ndi njuchi ili m'dziko la Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzayimbira mluzu cimphanga ciri m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Aigupto, ndi njuci iri m'dziko la Asuri.