Isaiah 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika m'zigwa zozama, m'ming'alu yam'matanthwe ndi pa zitsamba zonse zaminga, ndiponso pa mabusa onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.