Isaiah 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Banja lachifumu la ku Yuda litamva kuti dziko la Siriya lagwirizana ndi la Efuremu, mfumu pamodzi ndi anthu ake omwe adanjenjemera, monga m'mene mitengo yam'nkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efraimu. Ndipo mtima wace unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ace, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.