Isaiah 7:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe adzapeza ndithu mkaka wochuluka, mwakuti munthuyo azidzadya bwino kwambiri. Pakuti aliyense amene adzatsalire m'dzikomo azidzadya chambiko ndiponso uchi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo padzakhala, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo padzakhala, cifukwa ca kucuruka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uci adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko.