Isaiah 7:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsiku limenelo likadzafika, minda yamphesa yabwino, yomwe ili ndi mitengo yokwana chikwi m'munda uliwonse ndipo mtengo wake ndi masekeli siliva okwana chikwi chimodzi pa mtengo uliwonse, mudzamera a mkandankhuku ndi minga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti pali ponse panali mipesa cikwi cimodzi ya mtengo wace wa ndalama cikwi cimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.