Isaiah 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Yesaya kuti, “Tenga mwana wako Seari-Yasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku Munda wa Mmisiri Woyeretsa nsalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Tuluka tsopano kukachingamira Ahazi, iwe ndi Seari-Yasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamaliziro a mcherenje wa thamanda la pamtunda, kukhwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Turuka tsopano kukacingamira Ahazi, iwe ndi Seariyasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamariziro a mcerenje wa thamanda la pamtunda, ku khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru;