Isaiah 7:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukamuuze kuti achenjere, akhale phee, asaope, ndipo mtima wake usafooke chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi dziko lake la Siriya ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. Ameneŵa ali ngati zongofuka moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nukati kwa iye, Cenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, cifukwa ca zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, cifukwa ca mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.