Isaiah 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja dziko la Siriya limagonera pa likulu lake Damasiko, ndipo Damasiko amagonera pa mfumu yake Rezini. Kunena za Aefuremu, zisanapite zaka 65, adzaonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efuremu adzathyokathyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti Siriya amadalira Damasiko, ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi. Zisanathe zaka 65 Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efraimu adzatyokatyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;