Isaiah 8:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Usamachita nao zimene anthu ameneŵa amachita, ndipo usamaopa zimene iwowo amaopa, usachite nazo mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Usamanene kuti ndi chiwembu, chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu usamaope zimene anthuwa amaziopa, ndipo usamachite nazo mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musacinene, Ciwembu; ciri conse cimene anthu awa adzacinena, Ciwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musacite mantha.